Chichewa 14

  • ㆍISBN : 9788928239269
  • ㆍPages : 337

Paul C. Jong’s Kukula Mumzimu Mundandanda wa 3 - Kalata Woyamba Wa Yohane (Ⅰ)

Paul C. Jong

Mtumwi Yohane ndi mumodzi wa atsogoleri aakulu mumzimu mu Chikhristu. Makalata onse atatu iye analemba akuchitilabe umboni wa wa Choonadi wa cha poyera ndi mumzimu ku woyera mu Mpingo wa Mulungu. Koma muli ndime zina zimene ndi zikosa kuti ife timasulire ndi kumvetsa.
Tingapereke 1Yohane 1:8 ngati chisanzo cha ndime zobvuta mu Makalata ya Yohane: Tikanena kuti: “Tilibe uchimo,” ndiye kuti tikudzinamiza ndipo mwa ife mulibe choonadi.” Ndimeyi ndiyobvuta kumvetsa, maka-maka ngati taigwiritsa nchito ku okhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu.
Chisanzo chachiwiri ndi 1 Yohane 1:9, “Mulungu ndiwokhulupirika ndiponso wolungama, chotero tikavomereza machimo athu, adzatikhululukira ndi kutiyeretsa ku ntchito zonse zoipa.” Iyi yakhala ndime yakunenedwa pafupipafupi ngati ochimwa akufuna kupereka mfundo zabaibulo za mapemphero awo akulapa. Ndiyeno, ndimeyi ikutanthauza kuti ochimwa afunika kuvomereza machimo awo kuti akhululukidwe kumachimo awo amene anachita kodi? Kapena, kodi chikutanthauza kuti olungama amene okhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu ayenera kuvomereza machimo awo? Tifunika kukhulupilira ndimeyi malinga ndi kamsulidwe ka Mzimu Woyera, Mlembi wa Baibulo, ndiponso kumalingaliro a Mtumwi Yohane.
Chisanzo cha chitatu cha ndime yobvuta ndi 1 Yohane 2:22, “Kodi wabodza angakhalenso ndani, kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Khristu? Ameneyu ndiye wokana Khristu, amene amakana Atate ndi Mwana.” Ndimeyi ikulankhula za amene ndi adani a Mulungu. Ndimeyi ikufotokoza poyera kuti adani a Mulungu ndi onse aja sakhulupilira kuti Yesu ndi Mulungu. Ndipo ichi chikutanthauzanso kuti sakuthokoza Atate a Yesu Khristu ngati Mulungu.
Chachinayi ndi 1 Yohane 3:6 imene ikuti, “Yense wakukhala mwa Iye sachimwa yense wakuchimwa sanamuone Iye, ndipo sanamdziwe Iye.” Apa, ngati taona mawu, yense wakukhala mwa iye,” ndimeyi akuperekedwa ku olungama amene anayeretsedwa kumachimo awo onse mwa kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. Olungama sangakane chikhulupiliro chawo muzokhoma zilizonse cifukwa akukhulupilira mu uthenga woona. Kodi kungakhaledi ena amene sakuchita machimo ndi mathupi awo? Aliyense akuchita uchimo. Koma, okhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu sangachite uchimo otero ngati wakukana uthenga woona.

AUDIOBOOK
undefined
Due to COVID-19 and disruption to international mail service
we have temporally suspended our ‘Free Print Book service’.
In the light of this situation we are not able to mail you the books at this time.
Pray that this pandemic will end soon and the resumption of the postal service.