Chichewa 28

  • ㆍISBN : 9788928240234
  • ㆍPages : 442

Chimene Mulungu Mtatu AnaTIchitira Ife - Ziphunzitso pa Aefeso (II)

Paul C. Jong

Kodi Mkudziwa M’mene Ulili M’pingo wa Mulungu?  


Mwa kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, muyenera kukhala ndi maso anu akuuzimu masiku onse otseguka. Ngati munalandira chikhululukiro cha machimo anu mwa kukhulupilira moona mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndiye kuti mdzatha kuzindikira M'pingo wa Mulungu moyenera; apo bii, simukanatha kudziwa moyenera imene ndi mipingo yaboza.  

Masiku ano, Mulungu anakhazikitsa M'pingo Wake pachikhulupiliro cha okhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. M'pingo wa Mulungu ndi kusonkhana kwa aja amene anapulumutsidwa mwa kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. Chotero, ngati mitima yanu tsopano ili ndi chikhulupiliro mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndiye kuti kenako mungakhale ndi chikhulupiliro mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, kenako mungakhale moyo woona  wachikhulupiliro. Moyo otero wachikhulupiliro ndi wotheka mu M'pingo wa Mulungu mokha. Moonjezera, chikhulupiliro chotere chokha chikutiyeneretsa kukakhala kwa muyaya mu Ufumu wa Ambuye. Kupitira muchikhulupiliro ichi, tiyenera kulandira chikondi cha chipulumutso ndi madalitso onse auzimu a Kumwamba kuchokera kwa Mulungu Atate, kwa Yesu Khristu, ndi ku Mzimu Woyera. 

AUDIOBOOK
undefined
Due to COVID-19 and disruption to international mail service
we have temporally suspended our ‘Free Print Book service’.
In the light of this situation we are not able to mail you the books at this time.
Pray that this pandemic will end soon and the resumption of the postal service.