Chichewa 11
Choisissez votre format de fichier préféré et téléchargez-le en toute sécurité sur votre appareil mobile, PC ou tablette pour lire et écouter les collections de sermons n'importe quand et n'importe où. Tous les livres numériques et livres audio sont entièrement gratuits.
Bien que la pandémie de Covid-19 ait pris fin, il y a toujours des difficultés d`envoi ou réception de nos livres imprimés par la poste à cause de différentes situations internationales difficiles. Quand la situation internationale s`améliorera et que le courrier reviendra à la normale, nous reprendons l`envoi des livres imprimés.
Palibe njira yomwe winawake angapulumukire ndi kuthawa ku chiweruzo chamuyaya chifukwa cha machimo m’mitima mwao popanda Mpingo weniweni wa Mulungu(The New Life Mission), pakuti Chipulumutso cha Madzi ndi Mzimu chikupezeka, chimene chinakwiriridwa kalekalelo pambuyo pa imfa za atumwi, komanso kulephera kupilira kwa okhulupilira a Mpingo woyamba.
Ndikukhulupiliradi ndi kupemphera kuti inu mudzatenga Mau a choonadi a Madzi, Mwazi ndi Mzimu Olalikidwa ndi The New Life Mission monga kutseguka kwa khomo lanu kupita mu Ufumu wa Mulungu. Chifukwa chakuti ndi pokhulupilira mu Uthenga wa ubatizo wa Yesu(Pamene Iye anatenga machimo onse a dziko lapansi), kukhetsa Kwake kwa mwazi pa mtanda(pamene Iye analipira mphotho yonse ya uchimo) ndi pa kuuka Kwake kumene kudzera mwa uko Moyo Watsopano umaperekedwa kwa aliyense amene amakhulupilira kuti wina angalandiredi Mzimu wa Mulungu. Inde, palibe kukaikira kulikonse kuti munthu aliyense amafuna kutsogoleredwa ndi Mzimu, koma chinthu chifunika kwambiri kuganizira pamene mukulakala kutsogoleredwa ndi Mzimu ndi chakuti, ngati Mzimu amene inu mukuyesa kufunafuna kwenikweni ndi ochokeradi kwa Mulungu, ndipo ngati ndi ochokera kwa Mulungu, ndikofunika kudziwa momwe uwo umalandiridwira. Pakuti aneneri ambiri onyenga auka ndi mitundu yosiyanasiyana ya mizimu yoipa imene akunamizira nayo miyoyo yambiri yakhungu, iwo amalimbikira kuuza miyoyo yakhungu imeneyi kuti ipereke modzipereka mapephero ku mapiri modzadzidwa ndi zokumva zao zathupi poganizira mtanda wa Yesu, kulankhula m’malilime, kupereka mosalekeza mapemphero akulapa ndi kuvomera kuika manja kwa aneneri onyenga amenewa, monga njira yolandirira Mzimu wa Mulungu, zimene ndi zolakwika kwambiri. Choncho inu mumanyengedwa mosavuta ndi aneneri onyenga amenewa, chifukwa chakuti inu simukhulupilira mu uthenga wabwino wa choonadi wa Madzi ndi Mzimu wokhala ndi ubatizo wa Yesu kuchokera kwa Yohane, imfa Yake pa mtanda ndi kuuka Kwake zimene ndi chidziwitso cha choonadi chimene chidzalola inu kuti mulandire Mzimu wa Mulungu kuti udze kukhazikika mu mtima mwanu nthawi yomweyo pamene inu mwakhulupilira mu choonadi chimenechi cha Madzi, Mwazi ndi Mzimu. Pakuti Uthenga Wabwino wa choonadi umenewu wa madzi ndi Mzimu (Yohane 3:5) ndi Uthenga Wabwino umene umachotsa uchimo mu mtima wa aliyense amene amadzizindikira yekha kukhala ochimwa ndi kuvomera choonadi chimenechi pamene chafika kwa iye ndi mtima wodzichepetsa. Ndikupemphera ndi kuyembekeza kuti inu mudzaweruzana ndi Ambuye (Yesaya 1:18) pobwera ku tsamba lathu la pa intaneti www.bjnewlife.org ndi kudzidaunilodela nokha mabuku a pa intaneti aulere ndi mabuku omvera amene adzakuthandizani inu kulandira kutsuka kwa uchimo onse pamene inu mwakhulupilira mu uthenga wabwino wa choonadi wa Madzi ndi Mzimu ndipo kuyambira pamenepo, inu modziwikiratu mudzalandira Mzimu wa Mulungu.
Ulemelero ukhale kwa Mulungu tsopano ndi kosatha Ame.
Wogwira Nao Ntchito, Zambia