Chichewa 15

  • ㆍISBN : 9788928239450
  • ㆍPáginas : 391

Paul C. Jong’s Kukula Mumzimu Mundandanda wa 4 - Kalata Woyamba Wa Yohane (Ⅱ)

Paul C. Jong

Ngati ndiwe Mkristu woona, ufunika kudziwa chikondi cha kwambiri koposa mwa ziphunzitso chabe. Onse amene odziwa ndi kukhulupilira Yesu ngati M’pulumutsi wawo ayenera kudziwa chikondi cha Mulungu mwathunthu mu chikhululukiro chawo cha machimo cimene chinakwanilitsidwa kupitira mu Mawu a uthenga wa madzi ndi Mzimu. Tiyenera kukhala okhulupilira oona mu uthengawu oona kotero kuti tidziwe chikondi cha Mulungu mozama. Mu uthengau oona, chikondi cha Mulungu chikuvumbulutsidwa mwathunthu ndiponso mozama. Ngati tikufuna kudziwa Mulungu ngati chikondi, kuzindikira kwathu kuyenera kuchokera ku chikondi chathunthu cha Mulungu kwa ife cimene chinavumbulutsidwa mu Choonadi cha uthenga wa madzi ndi Mzimu. Ndipokhapo pamene tingatengere anthu ena ku chikondi choona cha Mulungu.
Monga mmene chinalembedwa mu Mawu a Mulungu, madzi akutanthauza ubatizo wa Yesu umene Iye analandira kwa Yohane M’batizi, ndipo mwazi akutanthauza chiweruzo cimene Iye analandira cifukwa cha machimo athu onse. Ndiponso, umboni wa chipulumutso chathu ukugona mu Mzimu Woyera, madzi, ndi mwazi (1 Yohane 5:8). Mautumiki a madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera ndi aja a Mulungu kupitira mu ameneo Iye anaombora ochimwa kumachimo awo onse.

Audiolivro
undefined
Devido ao COVID-19 e à interrupção do Serviço de Correio Internacional,
suspendemos temporariamente o nosso 'Serviço de Impressão Gratuita de Livros'.
Diante dessa situação, não podemos enviar os livros para você neste momento.
Ore para que esta pandemia termine em breve e retorne o serviço postal.