Chichewa 12

  • ㆍISBN : 9788928238859
  • ㆍPages : 406

ZIPHUNZITSO PA UTHENGA WA MATEYU (Ⅰ) - KODI N’NTHAWI YOTANI PAMENE MKRISTU ANGALANKHUZANE NDI AMBUYE MOMASUKA?

Paul C. Jong

Mtumwi Mateyu amatiuza kuti Mawu a Yesu analankhulidwa ku wina aliyense mdzikoli lapansi, pakuti iye anaona Yesu ngati Mfumu ya mafumu. Tsopano, Akristu mdziko lonse, amene angobadwa mwatsopano mwa kukuhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu umene timafalitsa, akufunitsitsadi kudya mkate wa moyo. Koma n’chobvuta kuti iwo akhale ndi chiyanjano limodzi ndi ife mu uthenga oona, cifukwa ali kutali kwambiri ndi ife.
Chotero, kuti tikwanilitse zosowa za anthuwa za Yesu Khristu, Mfumu ya mafumu, ziphunzitso mu bukuli zakonzedwa ngati mkate wa moyo watsopano kuti iwo alimbitse kukula kwawo kwauzimu. Mlembi akunena kuti onse amene analindira chikhululukiro cha machimo awo mwa kukhulupilira mu Mawu a Yesu Khristu, Mfumu ya mafumu, afunika kudya Mawu Ake oyera kotero kuti ateteze chikhulupiliro chawo ndiponso kupitilizabe miyoyo yawo yauzimu.
Bukuli lidzapereka mkate wauzimu weniweni wa moyo ku onse ainu amene anakhala anthu osatira Mfumu mwa chikhulupiliro. Kupitila mu M’pingo Wake ndiponso atumiki, Mulungu adzapitilizabe kumupatsani mkatewu wa umoyo. Lekani madalitso a Mulungu akhale pa inu nonse amene munabadwa mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu, amene ofunitsitsa kukhala ndi chiyanjano choona limodzi ndi ife mwa Khristu Yesu.

Audiolibros
undefined
Debido a COVID-19 y la interrupción del servicio de correo internacional,
hemos suspendido temporalmente nuestro "Servicio de Libros Impresos Gratis".
A la luz de esta situación no podemos enviarle los libros por correo en este momento.
Oren para que esta pandemia termine pronto y por la reanudación del servicio postal.