Zamkatimu
Mau Oyamba
CHAPITALA 21
1. Antchito Ogwiritsidwa Ntchito Ndi Mulungu (Mateyu 21:1-11)
2. Ndizolemekezeka kugwiritsidwa Ntchito mu Ntchito ya Ambuye (Mateyu 21:1-11)
3. Mudzati, “Ambuye Asowa Iwo” (Mateyu 21:1-14)
4. Choyambirira Komanso Chofunikira Kondani Mulungu (Mateyu 21:12-32)
5. Chiyanjano pakati pa Ntchito ya Yohane Mbatizi Ndi Uthenga Wabwino wa Chitetezero ku Machimo Athu (Mateyu 21:32)
6. Kuganiza Kwa Munthu Komwe Kumatsutsa Mulungu (Mateyu 21:44)
7. Atumiki Anzeru Zaumunthu Amatsutsa Uthenga Wabwino wa Yesu (Mateyu 21:44)
CHAPITALA 22
1. Okhawo Amene Abvala Chobvala cha Madzi ndi Mwazi Angapezeke ku Phwando la Kumwamba (Mateyu 22:1-14)
2. Fanizo la Phwando la Ukwati (Mateyu 22:1-14)
3. Bvalani Chobvala cha Chikhululukiro cha Machimo (Mateyu 22:1-14)
CHAPITALA 23
1. Atsogoleri Achinyengo ndi Akhungu (Mateyu 23:1-33)
CHAPITALA 24
1. Khalani ndi Chikhulupiliro Chomwe Chimakonzekera Kubwera Kwachiwiri kwa Ambuye Tsopano (Mateyu 24:1-8)
2. Konzekani za Kutha kwa Nthawi (Mateyu 24:3-14)
3. Tiyeni Tikhale Antchito Okhulupirika Kufikira Kumapeto (Mateyu 24:3-14)
Mtumwi Mateyu akutiuza ife kuti Mau a Yesu analankhulidwa kwa aliyense m’dziko lino, popeza Iye ankaona Yesu monga Mfumu ya mafumu. Tsopano, Akristu dziko lonse lapansi, amene angobadwa mwatsopano pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu omwe tikufalitsa, indedi akufunitsitsa kudya mkate wamoyo. Koma ndikobvuta kwa iwo kukhala ndi chiyanjano ndi ife mu uthenga wabwino weni weni, popeza iwo onse ali kutali ndi ife. Choncho, kuti tikumane ndi zofunika zauzimu za anthu amenewa a Yesu Kristu, Mfumu ya mafumu, ulaliki m’buku limeneli wakonzedwa monga mkate watsopano wa moyo kwa iwo kuti usamalire kukula kwao kwauzimu. Mlembi amanena kuti iwo amene alandira chikhululukiro cha machimo ao pokhulupilira m’Mau a Yesu Kristu, Mfumu ya mafumu, ayenera kudya Mau Ake angwiro pofuna kuteteza chikhulupiliro chao komanso kuchita bwino m’miyoyo yao yauzimu. Buku limeneli lidzapereka mkate weni weni wamoyo wauzimu kwa inu nonse amene mwakhala anthu olemekezeka a Mfumu mwa chikhulupiliro. Kudzera mu Mpingo Wake ndi akapolo Ake, Mulungu adzapitiriza kupereka kwa inu mkate umenewu wamoyo. Lolani madalitso a Mulungu akhale pa inu nonse amene mwabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, amene mukufuna kukhala ndi chiayanjano chauzimu ndi ife mwa Yesu Kristu.
更多