Rev. Paul C. Jong
ZAM’KATIMU
Chigawo choyamba – Maulaliki
1. Poyamba tiyenera kudziwa machimo athu kuti tipulumutsidwe (Marko 7:8-9, 20-23)
2. Anthu amabadwa ali Wochimwa (Marko 7:20-23)
3. Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi Lingatipulumutse Ife? (Luka 10:25-30)
4. Chiombolo cha muyaya (Yohane 8:1-12)
5. Ubatizo wa Yesu ndi Chitetezero Cha Machimo (Mateyu 3:13-17)
6. Yesu Anadza Mwa Madzi, Mwazi Ndi Mzimu (1 Yohane 5:1-12)
7. Ubatizo wa Yesu ndi Chifaniziro cha Chipulumutso cha Ochimwa (1 Petro 3:20-22)
8. Uthenga Wabwino wa Kusefukira Kwa Chitetezero cha Machimo (Yohane 13:1-17)
Chigawo chachiwiri – Mau owonjezera
1. Kulongosola kowonjezerapo
2. Mafunso ndi Mayankho
(Chichewa)
Phunziro la mutu waukulu umenewu ndi “kubadwanso mwatsopano mwa Madzi ndi Mzimu.” Wachokera pa phunziroli. Mwanjira ina, bukuli limatiuza ife momveka bwino kuti kubadwa mwatsopano ndi chiani komanso m’mene tingabadwire mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndendende malingana ndi Baibulo. Madzi amatanthauza ubatizo wa Yesu pa Yordano ndipo Baibulo limanena kuti machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu pamene Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Yohane anali woimilira mtundu onse wa anthu komanso wa pfuko la Aroni Mkulu wansembe. Aroni ankaika manja ake pamutu pa mbuzi yamoyo ndikupereka machimo a chaka chonse a Israyeli pa iyo pa Tsiku la Chitetezero. Ndi chithunzi cha zinthu zabwino ziri nkudza. Ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro cha kuika kwa manja.
Yesu anabatizidwa munjira yoika manja pa Yordano. Choncho Iye anachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake ndipo anapachikidwa kuti alipire machimo. Koma Akristu ambiri sadziwa chifukwa chimene Yesu anabatizidwira ndi Yohane Mbatizi mu Yordano. Ubatizo wa Yesu ndi mau osakira a bukuli, komanso gawo lofunika la Uthenga Wabwino wa Madzi ndi Mzimu. Tingabadwe mwatsopano pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi Mtanda Wake basi.
(English)
This title`s main subject is "to be born again of Water and the Spirit." It has the originality on the subject. In other words, this book clearly tells us what being born again is and how to be born again of water and the Spirit in strict accordance with the Bible. The water symbolizes the baptism of Jesus at the Jordan and the Bible says that all our sins were passed on to Jesus when He was baptized by John the Baptist. John was the representative of all mankind and a descendant of Aaron the High priest. Aaron laid his hands on the head of the scapegoat and passed all the yearly sins of the Israelites onto it on the Day of Atonement. It is a shadow of the good things to come. The baptism of Jesus is the antitype of the laying on of hands.
Jesus was baptized in the form of the laying on of hands at the Jordan. So He took away all the sins of the world through His baptism and was crucified to pay for the sins. But most Christians don`t know why Jesus was baptized by John the Baptist in the Jordan. Jesus` baptism is the keyword of this book, and the indispensable part of the Gospel of Water and the Spirit. We can be born again only by believing in the baptism of Jesus and His Cross.
Next
Chichewa 2: BWELERANI KU UTHENGA WABWINO WA MADZI NDI MZIMU