Zamkati
Kalambulabwalo
1. Kodi Ampatuko ndi Otani Pamaso pa Mulungu? (1 Mafumu 11:1-13)
2. Kodi Akristu Amene Akhulupilira Mwa Yesu Mkati mwa Chikonzero cha Nchito Yochokera Mkuganiza kwa Kuthupi Kwawo ndi Otani? (1 Mafumu 12:25-33)
3. Kutsatira Zokhumba za Thupi Kuzakupangitsa kukhala Wampatuko Nthawi Imeneyo (1 Mafumu 12:1-18)
4. Kodi ndi mu Uthenga Otani mu Umene Tsopano Mkukhulupilira? (1 Mafumu 13:33-34)
5. Akristu a Masiku Ano Amene Anachosapo Mulungu N’kuikapo Zinthu Zopanda Pake ndi Opembeza Mafano Pamaso pa Mulungu (1 Mafumu 11:1-13)
6. Kodi Mulungu Akupulumutsa Bwanji Ampatuko? (1 Mafumu 19:1-21)
7. Muyenera Kukhulupilira Kuti Yohane M’batizi ndi Oimilirako Anthu Onse (Mateyu 11:1-19)
8. Mitundu 7 ya Anthu Amene Adzatembeleledwa ndi Mulungu (Mateyu 23:1-36)
9. Chilitsani Madzi Oipa ndi Mchere (2 Mafumu 2:19-22)
Mu Baibulo, anthu a Isiraeli akunena kuti akupembeza Mulungu, koma pamapeto ake, anasatira Yerobowamu, anali kupembeza ana ang’ombe agolide. Mchoona, kopitila 2/3 ya mbiri ya Aisiraeli inali mbiri yakupembeza ana ang’ombe agolide, kuganiza kuti iwo ndi Mulungu. Pothera pake, ngakhalenso tsopanoli, akupitiliza kukhala ndi moyo kopanda kuzindikira choona kuti Yesu Khristu, amene anabwera kudzera mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, kuti ndi M’pulumutsi wawo oona. Kosasamala za ichi, kuli aYuda ambiri amene akuyembekezera za M’pulumutsi wawo, ngakhalenso tsopanoli.
Kodi ndiyeno, chikhulupiliro chanu inu amene mkunena kuti mkutengako mbali mu Chikristu Mnthawiyi ya Chipangano cha Tsopano chii motani? Kodi tsopano mkukhulupilira mu ndi kusatira Mulungu mwakumvetsetsa koyenera kwa Iye? Ngati ai, kodi mwina mwake inu si mkupembeza ana ang’ombe agolide mwakusamvetsetsa iwo ngati Mulungu? Ngati muli choncho, ndiye kuti muyenera kudziwa za choona chakuti mkupembeza fano pamaso pa Mulungu ngati anthu a Isiraeli. Ndiye kuti, muyenera kubweleranso ndi kukumana ndi Ambuye amene anabwera kudzera mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. Ndikhulupilira kuti mdzakwanitsa kukhulupilira mu Choonadi ngati mwazindikiradi pamaso pa Mulungu cimene ndi Choonadi cha chipulumutso mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, kodi si mdzatero?
Ndifuna kuchitira umboni pamaso pa inu chikhulupiliro choona ndi Choonadi pa chapamutu, “Ampatuko, Amene anasatira machimo a Yerobowamu.” Mwanjira zonse, Ndikhulupilira mdzakhala anthu a chikhulupiliro chofanana ngati chija changa.
更多