Zamkati
Mawu Oyamba
1. Chipulumutso Chathu Chinakonzedwa Mu Chilungamo cha Yesu Ngakhalenso Pamene Dziko Lisanakhazikitsidwe (Aefeso 1:1-4)
2. Takhala Akatundu a Mulungu mwa Chisomo Chake (Aefeso 1:1-14)
3. Tinapulumutsidwa Kupitira mu Chikondi ndi Nsembe ya Mulungu (Aefeso 1:1-6)
4. Tithokoza Mulungu Pakutiitana Ngati Mamembala a M’pingo Wake (Aefeso 1:20-23)
5. Tili Ndichiombolo Mogwirizana Ndi Chuma cha Chisomo cha Mulungu (Aefeso 1:7-14)
6. Kodi tinapangidwira Nchito Yolungama ya Ambuye? (Aefeso 2:1-10)
7. Tiyenera Kudziwa Mphamvu ndi Chisomo cha Mulungu mu Umoyo Wathu Wachikhulupiliro (Aefeso 2:1-22)
8. Kodi Tinali Mtundu wa Anthu Otani Pamaso pa Mulungu? (Aefeso 2:1-7)
9. Takhala Osadziwika Kwa Mulungu Atate Cifukwa cha Machimo Athu (Aefeso 2:14-22)
10. Madalitso Osaneneka a Khristu Ali M’mtima wa Oyera Aliyense Amene Akukhulupilira mu Uthenga wa Madzi ndi Mzimu (Aefeso 3:1-21)
11. Tetezani Chikhulupiliro Chanu mu Umoyo Wanu (Aefeso 4:1-6)
12. Tsanzirani Mulungu Ngati Ana Ake Okondedwa (Aefeso 5:1-2)
13. Musatengeko Mbali Kumachimo Adziko (Aefeso 5:1-14)
14. Kodi Kukhala mwa Kudzaza ndi Mzimu Chitanthauza Chiyani Kwenikweni? (Aefeso 5:1-21)
15. Iwo Amene Akukhala mwa Kudzaza ndi Mzimu (Afeso 5:15-21)
16. Tsutsanani ndi Machenjera a Satana (Aefeso 6:10-17)
Kodi Mkudziwa M’mene Ulili M’pingo wa Mulungu?
Mwa kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, muyenera kukhala ndi maso anu akuuzimu masiku onse otseguka. Ngati munalandira chikhululukiro cha machimo anu mwa kukhulupilira moona mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndiye kuti mdzatha kuzindikira M'pingo wa Mulungu moyenera; apo bii, simukanatha kudziwa moyenera imene ndi mipingo yaboza.
Masiku ano, Mulungu anakhazikitsa M'pingo Wake pachikhulupiliro cha okhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. M'pingo wa Mulungu ndi kusonkhana kwa aja amene anapulumutsidwa mwa kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. Chotero, ngati mitima yanu tsopano ili ndi chikhulupiliro mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndiye kuti kenako mungakhale ndi chikhulupiliro mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, kenako mungakhale moyo woona wachikhulupiliro. Moyo otero wachikhulupiliro ndi wotheka mu M'pingo wa Mulungu mokha. Moonjezera, chikhulupiliro chotere chokha chikutiyeneretsa kukakhala kwa muyaya mu Ufumu wa Ambuye. Kupitira muchikhulupiliro ichi, tiyenera kulandira chikondi cha chipulumutso ndi madalitso onse auzimu a Kumwamba kuchokera kwa Mulungu Atate, kwa Yesu Khristu, ndi ku Mzimu Woyera.
ပိုများသော